Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 113:2-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Lodala dzina la Yehova.Kuyambira tsopano kufikira kosatha.

3. Citurukire dzuwa kufikira kulowa kwaceLilemekezedwe dzina la Yehova.

4. Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse,Ulemerero wace pamwambamwamba.

5. Akunga Yehova Mulungu wathu ndani?Amene akhala pamwamba patali,

6. Nadzicepetsa apenyeZam'mwamba ndi za pa dziko lapansi.

7. Amene autsa wosauka lrumcotsa kupfumbi,Nakweza waumphawi kumcotsa kudzala.

8. Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu,Pamodzi ndi akulu a anthu ace.

9. Asungitsa nyumba mkazi wosaonamwana,Akhale mai wokondwera ndi ana.Haleluya.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 113