Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 112:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Wodala munthu wakudtira cifundo, nakongoletsa;Adzalimbika nao mlandu wace poweruzidwa.

6. Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse:Wolunguna adzakumbukika ku nthawi yosatha.

7. Sadzaopa mbiri yoipa;Mtima wace ngwokhazikika, wakhulupirira Yehova.

8. Mtima wace ngwocirikizika, sadzacita mantha,Kufikira ataona cofuna iye pa iwo omsautsa.

9. Anagawagawa, anapatsa aumphawi;Cilungamo cace cikhalitsa kosatha;Nyanga yace idzakwezeka ndi ulemu.

10. Woipa adzaziona, nadzapsa mtima;Adzakukuta mano, nadzasungunuka;Cokhumba oipa cidzatayika.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 112