Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 111:2-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Nchito za Yehova nzazikuru,Zofunika ndi onse akukondwera nazo.

3. Cocita Iye nca ulemu, ndi ukuru:Ndi cilungamo cace cikhalitsa kosatha.

4. Anacita cokumbukitsa zodabwiza zace;Yehova ndiye wa cisomo ndi nsoni zokoma.

5. Anapatsa akumuopa Iye cakudya;Adzakumbukila cipangano cace kosatha.

6. Anaonetsera anthu ace mphamvu ya nchito zace,Pakuwapatsa colowa ca amitundu.

7. Nchito za manja ace ndizo caonadi ndi ciweruzo;Malangizo ace onse ndiwo okhulupirika.

8. Acirikizika ku nthawi za nthawi,Acitika m'coonadi ndi cilunjiko,

9. Anatumizira anthu ace cipulumutso;Analamulira cipangano cace kosatha;Dzina lace ndilo loyera ndi loopedwa.

10. Kumuopa Yehova ndiko ciyambi ca nzeru;Onse akucita cotero ali naco cidziwitso cokoma;Cilemekezo cace cikhalitsa kosatha.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 111