1. Haleluya.Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse,Mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
2. Nchito za Yehova nzazikuru,Zofunika ndi onse akukondwera nazo.
3. Cocita Iye nca ulemu, ndi ukuru:Ndi cilungamo cace cikhalitsa kosatha.
4. Anacita cokumbukitsa zodabwiza zace;Yehova ndiye wa cisomo ndi nsoni zokoma.
5. Anapatsa akumuopa Iye cakudya;Adzakumbukila cipangano cace kosatha.
6. Anaonetsera anthu ace mphamvu ya nchito zace,Pakuwapatsa colowa ca amitundu.
7. Nchito za manja ace ndizo caonadi ndi ciweruzo;Malangizo ace onse ndiwo okhulupirika.