1. Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani pa dzanja lamanja langa,Kufikira nditaika adani anu copondapo mapazi anu.
2. Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kucokera ku Ziyoni;Citani ufumu pakati pa adani anu.
3. Anthu anu adzadzipereka eni ace tsiku la camuna canu:M'moyera mokometsetsa, mobadwira tnatanda kuca,Muli nae mame a ubwana wanu.
4. Yehova walamulira, ndipo sadzasintha,Inu ndinu wansembe kosathaMonga mwa cilongosoko ca Melikizedeke.
5. Yehova pa dzanja lamanja lakoAdzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wace.