Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 11:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndakhulupirira Yehova:Mutani nkunena kwa moyo wanga,Thawirani ku phiri lanu ngati mbalame?

2. Pakuti, onani, oipa akoka uta,Apiringidza mubvi wao pansinga,Kuwaponyera mumdima oongoka mtima.

3. Akapasuka maziko,Wolungama angacitenji?

4. Yehova ali m'Kacisi wace woyera,Yehova, mpando wacifumu wace uli m'Mwamba;Apenyerera ndi maso ace, ayesa ana a anthu ndi zikope zace.

5. Yehova ayesa wolungama mtima:Koma moyo wace umuda woipa ndi iye wakukonda ciwawa.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 11