Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 108:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Wakhazikika mtima wanga, Mulungu;Ndidzayimba, inde ndidzayimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga.

2. Galamukani, cisakasa ndi zeze;Ndidzauka ndekha mamawa.

3. Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova:Ndipo ndidzayimba zakukulemekezani mwa anthu.

4. Pakuti cifundo canu ncacikuru kupitirira kumwamba,Ndi coonadi canu kufikira mitambo.

5. Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu;Ndi ulemerero wanu pamwamba pa dziko lonse lapansi.

6. Kuti okondedwa anu alanditsidwe,Pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutibvomereze.

7. Mulungu analankhula m'ciyero cace; ndidzakondwerera:Ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso cigwa ca Sukoti.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 108