Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 107:28-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Pamenepo apfuulira kwa Yehova m'kusauka kwao,Ndipo awaturutsa m'kupsinjika kwao.

29. Asanduliza namondwe akhale bata,Kotero kuti mafunde ace atonthole.

30. Pamenepo akondwera, popeza pagwabata;Ndipo Iye awatsogolera kudooko afumko.

31. Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!

32. Amkwezenso mu msonkhano wa anthu,Namlemekeze pokhala akulu.

33. Asanduliza mitsinje ikhale cipululu,Ndi akasupe a madzi akhale nthaka youma;

34. Dziko lazipatso, likhale lakhulo,Cifukwa ca coipa ca iwo okhalamo.

35. Asanduliza cipululu cikhale tha wale,Ndi dziko louma likhale akasupe a madzi.

36. Ndi apo akhalitsa anjala,Kuti amangeko mudzi wokhalamo anthu;

37. Nafese m'minda, naoke mipesa,Ndiyo vakubata zipatso zolemeza.

38. Ndipo awadalitsa, kotero kuti, acuruka kwambiri;Osacepsanso zoweta zao.

39. Koma acepanso, nawerama,Cifukwa ca cisautso, coipa ndi cisoni.

40. Atsanulira cimpepulo pa akulu,Nawasokeretsa m'cipululu mopanda njira.

41. Koma aika waumphawi pamsanje posazunzika,Nampatsa mabanja ngati gulu la nkhosa.

42. Oongoka mtima adzaciona nadzasekera;Koma cosalungama conse citseka pakamwa pace.

43. Wokhala nazo nzeru asamalire izi,Ndipo azindikire zacifundo za Yehova,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 107