28. Pamenepo apfuulira kwa Yehova m'kusauka kwao,Ndipo awaturutsa m'kupsinjika kwao.
29. Asanduliza namondwe akhale bata,Kotero kuti mafunde ace atonthole.
30. Pamenepo akondwera, popeza pagwabata;Ndipo Iye awatsogolera kudooko afumko.
31. Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!
32. Amkwezenso mu msonkhano wa anthu,Namlemekeze pokhala akulu.
33. Asanduliza mitsinje ikhale cipululu,Ndi akasupe a madzi akhale nthaka youma;
34. Dziko lazipatso, likhale lakhulo,Cifukwa ca coipa ca iwo okhalamo.
35. Asanduliza cipululu cikhale tha wale,Ndi dziko louma likhale akasupe a madzi.
36. Ndi apo akhalitsa anjala,Kuti amangeko mudzi wokhalamo anthu;
37. Nafese m'minda, naoke mipesa,Ndiyo vakubata zipatso zolemeza.
38. Ndipo awadalitsa, kotero kuti, acuruka kwambiri;Osacepsanso zoweta zao.
39. Koma acepanso, nawerama,Cifukwa ca cisautso, coipa ndi cisoni.