Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 107:22-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo apereke nsembe zaciyamiko,Nafotokozere nchito zace ndi kupfuula mokondwera.

23. Iwo akutsikira kunyanja nalowa m'zombo,Akucita nchito zao pa madzi akuru;

24. Iwowa apenya nchito za Yehova,Ndi zodabwiza zace m'madzi ozama.

25. Popeza anena, nautsa namondwe,Amene autsa mafunde ace.

26. Akwera kuthambo, atsikira kozama;Mtima wao usungunuka naco coipaco.

27. Adzandira napambanitsa miyendo ngati munthu woledzeta,Nathedwa nzeru konse.

28. Pamenepo apfuulira kwa Yehova m'kusauka kwao,Ndipo awaturutsa m'kupsinjika kwao.

29. Asanduliza namondwe akhale bata,Kotero kuti mafunde ace atonthole.

30. Pamenepo akondwera, popeza pagwabata;Ndipo Iye awatsogolera kudooko afumko.

31. Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!

32. Amkwezenso mu msonkhano wa anthu,Namlemekeze pokhala akulu.

33. Asanduliza mitsinje ikhale cipululu,Ndi akasupe a madzi akhale nthaka youma;

34. Dziko lazipatso, likhale lakhulo,Cifukwa ca coipa ca iwo okhalamo.

35. Asanduliza cipululu cikhale tha wale,Ndi dziko louma likhale akasupe a madzi.

36. Ndi apo akhalitsa anjala,Kuti amangeko mudzi wokhalamo anthu;

37. Nafese m'minda, naoke mipesa,Ndiyo vakubata zipatso zolemeza.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 107