Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 107:2-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Atere oomboledwa a Yehova,Amene anawaombola m'dzanja la wosautsa;

3. Nawasokolotsa kumaiko,Kucokera kum'mawa ndi kumadzulo,Kumpoto ndi kunyanja.

4. Anasokera m'cipululu, m'njira yopanda anthu;Osapeza mudzi wokhalamo.

5. Anamva njala ndi ludzu,Moyo wao unakomoka m'kati mwao.

6. Pamenepo anapfuulira kwa Yehova mumsauko mwao,Ndipo anawalanditsa m'kupsinjika kwao.

7. Ndipo anawatsogolera pa njira yolunjika,Kuti amuke ku mudzi wokhalamo.

8. Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!

9. Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka,Nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.

10. Iwo akukhala mumdima ndi mu mthunzi wa imfa,Omangika ndi kuzunzika ndi citsulo;

11. Popeza anapikisana nao mau a Mulungu,Napeputsa uphungu wa Wam'mwambamwamba;

12. Kotero kuti anagonjetsa mtima wao ndi cobvuta;Iwowa anakhumudwa koma panalibe mthandizi.

13. Pamenepo anapfuulira kwa Yehova mumsauko mwao,Ndipo anawapulumutsa m'kupsinjika kwao.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 107