Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 107:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Popeza anapikisana nao mau a Mulungu,Napeputsa uphungu wa Wam'mwambamwamba;

12. Kotero kuti anagonjetsa mtima wao ndi cobvuta;Iwowa anakhumudwa koma panalibe mthandizi.

13. Pamenepo anapfuulira kwa Yehova mumsauko mwao,Ndipo anawapulumutsa m'kupsinjika kwao.

14. Anawaturutsa mumdima ndi mu mthunzi wa imfa,Nadula zomangira zao.

15. Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!

16. Popeza adaswa zitseko zamkuwa,Natyola mipiringidzo yacitsulo.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 107