7. Makolo athu sanadziwitsa zodabwiza zanu m'Aigupto;Sanakumbukila zacifundo zanu zaunyinji;Koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.
8. Koma anawapulumutsa cifukwa ca dzina lace,Kuti adziwitse cimphamvu cace.
9. Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, niiphwa:Potero anawayendetsa mozama ngati m'cipululu.
10. Ndipo anawapulumutsa m'dzanja la iye amene anawada,Nawaombola ku dzanja la mdani.
11. Ndipo madziwo anamiza owasautsa;Sanatsala mmodzi yense.
12. Pamenepo anabvomereza mau ace;Anayimbira comlemekeza.
13. Koma anaiwala nchito zace msanga;Sanalindira uphungu wace:
14. Popeza analaka-lakatu kucidikhako,Nayesa Mulungu m'cipululu.
15. Ndipo anawapatsa copempha iwo;Koma anaondetsa mitima yao.
16. Ndipo kumisasa anacita nao nsanje MoseNdi Aroni woyerayo wa Yehova.
17. Dziko lidayasama nilidameza Datani,Ndipo linafotsera gulu la Abiramu.