5. Kuti ndione cokomaco ca osankhika anu,Kuti ndikondwere naco cikondwerero ca anthu anu,Kuti ndidzitamandire pamodzi ndi colowa canu.
6. Talakwa pamodzi ndi makolo athu;Tacita mphulupulu, tacita coipa.
7. Makolo athu sanadziwitsa zodabwiza zanu m'Aigupto;Sanakumbukila zacifundo zanu zaunyinji;Koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.
8. Koma anawapulumutsa cifukwa ca dzina lace,Kuti adziwitse cimphamvu cace.
9. Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, niiphwa:Potero anawayendetsa mozama ngati m'cipululu.
10. Ndipo anawapulumutsa m'dzanja la iye amene anawada,Nawaombola ku dzanja la mdani.
11. Ndipo madziwo anamiza owasautsa;Sanatsala mmodzi yense.