Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 106:44-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

44. Koma anapenya nsautso yao,Pakumva kupfuula kwao:

45. Ndipo anawakumbukila cipangano cace,Naleza monga mwa kucuruka kwa cifundo cace.

46. Ndipo anawacitira kuti apeze nsoniPamaso pa onse amene adawamanga ndende.

47. Tipulumutseni, Yehova, Mulungu wathu,Ndi kutisokolotsa kwa amitundu,Kuti tiyamike dzina lanu loyera,Ndi kudzitamandira naco cilemekezo canu.

48. Wodala Yehova, Mulungu wa Israyeli,Kuyambira kosayamba kufikira kosatha.Ndi anthu onse anene, Amen.Haleluya,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 106