Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 106:32-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Anautsanso mkwiyo wace ku madzi a Meriba,Ndipo kudaipira Mose cifukwa ca iwowa:

33. Pakuti anawawitsa mzimu wace,Ndipo analankhula zosayenera ndi milomo yace.

34. Sanaononga mitunduyo ya anthu,Imene Mulungu adawauza;

35. Koma anasokonekerana nao amitundu,Naphunzira nchito zao:

36. Ndipo anatumikira mafano ao,Amene anawakhalira msampha:

37. Ndipo anapereka ana ao amuna ndi akazi nsembe ya kwa ziwanda,

38. Nakhetsa mwazi wosacimwa, ndi wo mwazi wa ana ao amuna ndi akazi,Amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani;M'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.

39. Ndipo anadziipsa nazo nchito zao,Nacita cigololo nao macitidwe ao.

40. Potero udayaka mkwiyo wa Yehova pa anthu ace,Nanyansidwa Iye ndi colowa cace.

41. Ndipo anawapereka m'manja a amitundu;Ndipo odana nao anacita ufumu pa iwo.

42. Adani ao anawasautsanso,Nawagonjetsa agwire mwendo wao.

43. Iye anawalanditsa kawiri kawiri;Koma anapikisana ndi Iye mwa uphungu wao,Ndi mphulupulu zao zinawafoketsa,

44. Koma anapenya nsautso yao,Pakumva kupfuula kwao:

45. Ndipo anawakumbukila cipangano cace,Naleza monga mwa kucuruka kwa cifundo cace.

46. Ndipo anawacitira kuti apeze nsoniPamaso pa onse amene adawamanga ndende.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 106