Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 106:30-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Pamenepo panauka Pinehasi, nacita cilango:Ndi mliriwo unaletseka.

31. Ndipo adamuyesa iye wacilungamo,Ku mibadwo mibadwo ku nthawi zonse.

32. Anautsanso mkwiyo wace ku madzi a Meriba,Ndipo kudaipira Mose cifukwa ca iwowa:

33. Pakuti anawawitsa mzimu wace,Ndipo analankhula zosayenera ndi milomo yace.

34. Sanaononga mitunduyo ya anthu,Imene Mulungu adawauza;

35. Koma anasokonekerana nao amitundu,Naphunzira nchito zao:

36. Ndipo anatumikira mafano ao,Amene anawakhalira msampha:

37. Ndipo anapereka ana ao amuna ndi akazi nsembe ya kwa ziwanda,

38. Nakhetsa mwazi wosacimwa, ndi wo mwazi wa ana ao amuna ndi akazi,Amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani;M'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.

39. Ndipo anadziipsa nazo nchito zao,Nacita cigololo nao macitidwe ao.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 106