27. Kugwetsanso mbeu zao mwa amitundu,Ndi kuwabalalitsa m'maiko maiko.
28. Ndipo anadzipatikiza ndi BaalaPeori,Nadyanso nsembe za akufa.
29. Ndipo anamkwiyitsa nazo zocita zao;Kotero kuti mliri unawagwera.
30. Pamenepo panauka Pinehasi, nacita cilango:Ndi mliriwo unaletseka.
31. Ndipo adamuyesa iye wacilungamo,Ku mibadwo mibadwo ku nthawi zonse.
32. Anautsanso mkwiyo wace ku madzi a Meriba,Ndipo kudaipira Mose cifukwa ca iwowa:
33. Pakuti anawawitsa mzimu wace,Ndipo analankhula zosayenera ndi milomo yace.
34. Sanaononga mitunduyo ya anthu,Imene Mulungu adawauza;
35. Koma anasokonekerana nao amitundu,Naphunzira nchito zao:
36. Ndipo anatumikira mafano ao,Amene anawakhalira msampha:
37. Ndipo anapereka ana ao amuna ndi akazi nsembe ya kwa ziwanda,