Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 106:24-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Anapeputsanso dziko lofunika,Osabvomereza mau ace;

25. Koma anadandaula m'mahema mwao,Osamvera mau a Yehova.

26. Potero anawasamulira dzanja lace,Kuti awagwetse m'cipululu:

27. Kugwetsanso mbeu zao mwa amitundu,Ndi kuwabalalitsa m'maiko maiko.

28. Ndipo anadzipatikiza ndi BaalaPeori,Nadyanso nsembe za akufa.

29. Ndipo anamkwiyitsa nazo zocita zao;Kotero kuti mliri unawagwera.

30. Pamenepo panauka Pinehasi, nacita cilango:Ndi mliriwo unaletseka.

31. Ndipo adamuyesa iye wacilungamo,Ku mibadwo mibadwo ku nthawi zonse.

32. Anautsanso mkwiyo wace ku madzi a Meriba,Ndipo kudaipira Mose cifukwa ca iwowa:

33. Pakuti anawawitsa mzimu wace,Ndipo analankhula zosayenera ndi milomo yace.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 106