21. Anaiwala Mulungu mpulumutsi wao,Amene anacita zazikulu m'Aigupto;
22. Zodabwiza m'dziko la Hamu,Zoopsa ku Nyanja Yofiira.
23. Potero Iye adati awaononge,Pakadapanda Mose wosankhika wace, kuima pamaso pace pagamukapo,Kubweza ukali wace ungawaononge,
24. Anapeputsanso dziko lofunika,Osabvomereza mau ace;
25. Koma anadandaula m'mahema mwao,Osamvera mau a Yehova.
26. Potero anawasamulira dzanja lace,Kuti awagwetse m'cipululu:
27. Kugwetsanso mbeu zao mwa amitundu,Ndi kuwabalalitsa m'maiko maiko.
28. Ndipo anadzipatikiza ndi BaalaPeori,Nadyanso nsembe za akufa.
29. Ndipo anamkwiyitsa nazo zocita zao;Kotero kuti mliri unawagwera.
30. Pamenepo panauka Pinehasi, nacita cilango:Ndi mliriwo unaletseka.
31. Ndipo adamuyesa iye wacilungamo,Ku mibadwo mibadwo ku nthawi zonse.