14. Popeza analaka-lakatu kucidikhako,Nayesa Mulungu m'cipululu.
15. Ndipo anawapatsa copempha iwo;Koma anaondetsa mitima yao.
16. Ndipo kumisasa anacita nao nsanje MoseNdi Aroni woyerayo wa Yehova.
17. Dziko lidayasama nilidameza Datani,Ndipo linafotsera gulu la Abiramu.
18. Ndipo m'gulu mwao mudayaka moto;Lawi lace lidapsereza oipawo.
19. Anapanga mwana wa ng'ombe ku Horebu,Nagwadira fano loyenga.
20. M'mwemo anasintha ulemerero waoNdi fanizo la ng'ombe Yakudya msipu.