Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 106:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Haleluya.Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino:Pakuti cifundo cace ncosatha.

2. Adzafotokoza ndani nchito zamphamvu za Yehova,Adzamveketsa ndani cilemekezo cace conse?

3. Odala iwo amene asunga ciweruzo,Iye amene acita cilungamo nthawi zonse.

4. Mundikumbukile, Yehova, monga momwe mubvomerezana ndi anthu anu;Mundionetsa cipulumutso canu:

5. Kuti ndione cokomaco ca osankhika anu,Kuti ndikondwere naco cikondwerero ca anthu anu,Kuti ndidzitamandire pamodzi ndi colowa canu.

6. Talakwa pamodzi ndi makolo athu;Tacita mphulupulu, tacita coipa.

7. Makolo athu sanadziwitsa zodabwiza zanu m'Aigupto;Sanakumbukila zacifundo zanu zaunyinji;Koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.

8. Koma anawapulumutsa cifukwa ca dzina lace,Kuti adziwitse cimphamvu cace.

9. Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, niiphwa:Potero anawayendetsa mozama ngati m'cipululu.

10. Ndipo anawapulumutsa m'dzanja la iye amene anawada,Nawaombola ku dzanja la mdani.

11. Ndipo madziwo anamiza owasautsa;Sanatsala mmodzi yense.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 106