35. Ndipo zinadya zitsamba zonse za m'dziko mwao,Zinadyanso zipatso za m'nthaka mwao.
36. Ndipo Iye anapha acisamba onse m'dziko mwaoCoyambira ca mphamvu yao yonse.
37. Ndipo anawaturutsa pamodzi ndi siliva ndi golidi:Ndi mwa mafuko ao munalibe mmodzi wokhumudwa.
38. Aigupto anakondwera pakucoka iwo;Popeza kuopsa kwao kudawagwera.
39. Anayala mtambo uwaphimbe;Ndi moto uunikire usiku,
40. Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri.Nawakhuritsa mkate wakumwamba.
41. Anatsegula pathanthwe, anaturukamo madzi;Nayenda pouma ngati mtsinje.