Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 105:31-45 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Ananena, ndipo inadza mitambo ya nchenche,Ndi nsabwe kufikira m'malire ao onse.

32. Anawapatsa mvula yamatalala,Lawi la moto m'dziko lao.

33. Ndipo anapanda mipesa yao, ndi mikuyu yao;Natyola mitengo kufikira m'malire ao onse.

34. Ananena, ndipo linadza dzombeNdi mphuci, ndizo zosawerengeka,

35. Ndipo zinadya zitsamba zonse za m'dziko mwao,Zinadyanso zipatso za m'nthaka mwao.

36. Ndipo Iye anapha acisamba onse m'dziko mwaoCoyambira ca mphamvu yao yonse.

37. Ndipo anawaturutsa pamodzi ndi siliva ndi golidi:Ndi mwa mafuko ao munalibe mmodzi wokhumudwa.

38. Aigupto anakondwera pakucoka iwo;Popeza kuopsa kwao kudawagwera.

39. Anayala mtambo uwaphimbe;Ndi moto uunikire usiku,

40. Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri.Nawakhuritsa mkate wakumwamba.

41. Anatsegula pathanthwe, anaturukamo madzi;Nayenda pouma ngati mtsinje.

42. Popeza anakumbukila mau ace oyera,Ndi Abrahamu mtumiki wace.

43. Potero anaturutsa anthu ace ndi kusekerera,Osankhika ace ndi kupfuula mokondwera.

44. Ndipo anawapatsa maiko a amitundu;Iwo ndipo analanda zipatso za nchito ya anthu:

45. Kuti asamalire malemba ace,Nasunge malamulo ace.Haleluya.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 105