Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 105:18-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Anapweteka miyendo yace ndi matangadza;Anamgoneka m'unyolo;

19. Kufikira nyengo yakucitika maneno ace;Mau a Yehova anamuyesa.

20. Mfumuyo anatuma munthu nammasula;Woweruza mitundu ya anthu anamtsegulira.

21. Anamuika akhale woyang'anira nyumba yace,Ndi woweruza wa pa zace zonse:

22. Amange nduna zace iye mwini,Alangize akulu ace adziwe nzeru.

23. Pamenepo Israyeli analowa m'Aigupto;Ndi Yakobo anakhala mlendo m'dziko la Hamu.

24. Ndipo anacurukitsatu mtundu wa anthu ace,Nawapatsa mphamvu yoposa owasautsa.

25. Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ace,Kuti acite monyenga ndi atumiki ace.

26. Anatuma Mose mtumiki wace, Ndi Aroni amene adamsankha.

27. Anaika pakati pao zizindikilo zace,Ndi zodabwiza m'dziko la Hamu.

28. Anatumiza mdima ndipo kunada;Ndipo sanapikisana nao mau ace.

29. Anasanduliza madzi ao akhale mwazi,Naphanso nsomba zao.

30. Dziko lao linacuruka acule,M'zipinda zomwe za mafumu ao.

31. Ananena, ndipo inadza mitambo ya nchenche,Ndi nsabwe kufikira m'malire ao onse.

32. Anawapatsa mvula yamatalala,Lawi la moto m'dziko lao.

33. Ndipo anapanda mipesa yao, ndi mikuyu yao;Natyola mitengo kufikira m'malire ao onse.

34. Ananena, ndipo linadza dzombeNdi mphuci, ndizo zosawerengeka,

35. Ndipo zinadya zitsamba zonse za m'dziko mwao,Zinadyanso zipatso za m'nthaka mwao.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 105