Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 102:13-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Inu mudzauka, ndi kucitira nsoni Ziyoni;Popeza yafika nyengo yakumcitira cifundo, nyengo yoikika.

14. Pakuti atumiki anu akondwera nayo miyala yace,Nacitira cifundo pfumbi lace.

15. Pamenepo amitundu adzaopa dzina la Yehova,Ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu;

16. Pakuti Yehova anamanga Ziyoni,Anaoneka m'ulemerero wace;

17. Anasamalira pemphero la iwo akusowa konse,Osapepula pemphero lao.

18. Ici adzacilembera mbadwo ukudza;Ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.

19. Pakuti anapenya pansi ali kumwamba kuli malo ace opatulika;Yehova pokhala kumwamba anapenya dziko lapansi;

20. Kuti amve kubuula kwa wandende;Namasule ana a imfa,

21. Kuti anthu alalikire dzina la Yehova m'Ziyoni,Ndi cilemekezo cace m'Yerusalemu;

22. Posonkhana pamodzi mitundu ya anthu,Ndi maufumu kuti atumikire Yehova.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 102