Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 101:5-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Wakuneneza mnzace m'tseri ndidzamdula;Wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.

6. Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine;Iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.

7. Wakucita cinyengo sadzakhala m'kati mwa nyumba yanga;Wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.

8. Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko;Kuduliratu onse akucita zopanda pace ku mudzi wa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 101