1. Ndidzayimba za cifundo ndi ciweruzo;Ndidzayimba zakukulemekezani Inu, Yehova.
2. Ndidzacita mwanzeru m'njira yangwiro;Mudzandidzera liti?Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.
3. Sindidzaika cinthu coipa pamaso panga;Cocita iwo akupatuka padera cindiipira;Sicidzandimamatira.
4. Mtima wopulukira udzandicokera;Sindidzadziwana naye woipa.
5. Wakuneneza mnzace m'tseri ndidzamdula;Wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.