Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 10:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yace, akuti, Sadzafunsira.Malingaliro ace onse akuti, Palibe Mulungu.

5. Mayendedwe ace alimbika nthawi zonse;Maweruzo anu ali pamwamba posaona iye;Adani ace onse awanyodola.

6. Ati mumtima mwace, Sindidzagwedezeka ine;Ku mibadwo mibadwo osagwa m'tsoka ine.

7. M'kamwa mwace mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kucenjerera;Pansi pa lilime lace pali cibvutitso copanda pace.

8. Akhala m'molalira midzi;Mobisalamo akupha munthu wosacimwa:Ambisira waumphawi nkhope yace,

9. Alalira monga mkango m'ngaka mwace;Alalira kugwira wozunzika:Agwira wozunzika, pakumkola m'ukonde mwace.

10. Aunthama, nawerama,Ndipo aumphawi agwa m'zala zace.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 10