Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 10:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Muimiranji patari, Yehova?Mubisaliranji m'nyengo za nsautso?

2. Podzikuza woipa apsereza waumphawi;Agwe m'ciwembu anapanganaco.

3. Pakuti woipa adzitamira cifuniro ca moyo wace,Adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.

4. Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yace, akuti, Sadzafunsira.Malingaliro ace onse akuti, Palibe Mulungu.

5. Mayendedwe ace alimbika nthawi zonse;Maweruzo anu ali pamwamba posaona iye;Adani ace onse awanyodola.

6. Ati mumtima mwace, Sindidzagwedezeka ine;Ku mibadwo mibadwo osagwa m'tsoka ine.

7. M'kamwa mwace mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kucenjerera;Pansi pa lilime lace pali cibvutitso copanda pace.

8. Akhala m'molalira midzi;Mobisalamo akupha munthu wosacimwa:Ambisira waumphawi nkhope yace,

9. Alalira monga mkango m'ngaka mwace;Alalira kugwira wozunzika:Agwira wozunzika, pakumkola m'ukonde mwace.

10. Aunthama, nawerama,Ndipo aumphawi agwa m'zala zace.

11. Anena m'mtima mwace, Mulungu waiwala;Wabisa nkhope yace; sapenya nthawi zonse,

12. Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu;Musaiwale ozunzika.

13. Woipa anyozeranii Mulungu,Anena m'mtima mwace, Simudzafunsira?

Werengani mutu wathunthu Masalmo 10