Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 3:54-66 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

54. Madzi anayenda pamwamba pa mutu panga, ndinati, dalikhidwa.

55. Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndiri m'dzenje lapansi;

56. Munamva mau anga; musabise khutu lanu popuma ndi popfuulaine.

57. Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati, Usaope.

58. Ambuye munanenera moyo wanga mirandu yace; munaombola moyo wanga.

59. Yehova, mwaona coipa anandicitiraco, mundiweruzire;

60. Mwaona kubwezera kwao konse ndi zopangira zao zonse za pa ine.

61. Mwamva citonzo cao, Yehova, ndi zopangira zao zonse za pa ine,

62. Milomo ya akutsutsana nane ndi zolingalira zao za pa ine tsiku lonse.

63. Taonani kukhala ndi kunyamuka kwao; ndine nyimbo yao.

64. Mudzawabwezera cilango, Yehova, monga mwa macitidwe a manja ao;

65. Muphimbe mtima wao ndi kuwatemberera;

66. Mudzawalondola mokwiya ndi kuwaononga pansi pa thambo la Yehova.

Werengani mutu wathunthu Maliro 3