Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 3:45-57 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

45. Mwatiika pakati pa amitundu ngati zinyalala ndi za kudzala.

46. Adani athu onse anatiyasamira,

47. Mantha ndi dzenje zitifikira, ndiphokose ndi cionongeko.

48. M'diso mwanga mutsikamitsinje ya madzi cifukwa ca mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga woonongedwa,

49. Diso langa lingotsanulira osaleka, osapumula,

50. Kufikira Yehova adzazolika kumwamba ndi kuona;

51. Diso langa limvetsa moyo wanga zowawa cifukwa ca ana akazi onse a m'mudzi mwanga.

52. Ondida opanda cifukwa anandiinga ngati mbalame;

53. Anaononga moyo wanga m'dzenje, naponya mwala pamwambapaine;

54. Madzi anayenda pamwamba pa mutu panga, ndinati, dalikhidwa.

55. Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndiri m'dzenje lapansi;

56. Munamva mau anga; musabise khutu lanu popuma ndi popfuulaine.

57. Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati, Usaope.

Werengani mutu wathunthu Maliro 3