Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 3:26-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha cipulumutso ca Yehova.

27. Nkokoma kuti munthu asenze gori ali wamng'ono.

28. Akhale pa yekha, natonthole, pakuti Mulungu wamsenzetsa ilo.

29. Aike kamwa lace m'pfumbi; kapena ciripo ciyembekezo.

30. Atembenuzire wompanda tsaya lace, adzazidwe ndi citonzo.

31. Pakuti Yehova sadzataya kufikira nthawi zonse,

32. Angakhale aliritsa, koma adzacitira cisoni monga mwa kucuruka kwa zifundo zace.

33. Pakuti samasautsa dala, ngakhale kumvetsa ana a anthu cisoni.

34. Kupondereza andende onse a m'dziko,

35. Kupambutsa ciweruzo ca munthu pamaso pa Wam'mwambamwamba,

36. Kukhotetsa mlandu wa munthu, zonsezi Ambuye sazikonda.

37. Ndani anganene, conena cace ndi kucitikadi, ngati Ambuye salamulira?

38. Kodi m'kamwa mwa Wam'mwambamwamba simuturuka zobvuta ndi zabwino?

39. Kodi munthu wamoyo adandauliranji pokhala m'zocimwa zace?

40. Tisanthule ntiyese njira zathu ntibwerenso kwa Yehova.

41. Titukulire mitima yathu ndi, manja athu omwe kwa Mulungu ali kumwamba.

42. Ife tilakwa ndi kupikisana nanu, ndipo Inu simunatikhululukira.

43. Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola, mwatipha osacitira cisoni.

44. Mwadzikuta ndi mtambo kuti pemphero lathu lisapyolemo.

45. Mwatiika pakati pa amitundu ngati zinyalala ndi za kudzala.

46. Adani athu onse anatiyasamira,

Werengani mutu wathunthu Maliro 3