Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 3:22-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Cifukwa cakusathedwa ife ndico cifundo ca Yehova, pakuti cisoni cace sicileka;

23. Cioneka catsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.

24. Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova; cifukwa cace ndidzakhulupirira.

25. Yehova akhalira wabwino omlindirira, ndi moyo womfunafuna.

26. Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha cipulumutso ca Yehova.

27. Nkokoma kuti munthu asenze gori ali wamng'ono.

28. Akhale pa yekha, natonthole, pakuti Mulungu wamsenzetsa ilo.

29. Aike kamwa lace m'pfumbi; kapena ciripo ciyembekezo.

30. Atembenuzire wompanda tsaya lace, adzazidwe ndi citonzo.

31. Pakuti Yehova sadzataya kufikira nthawi zonse,

32. Angakhale aliritsa, koma adzacitira cisoni monga mwa kucuruka kwa zifundo zace.

33. Pakuti samasautsa dala, ngakhale kumvetsa ana a anthu cisoni.

34. Kupondereza andende onse a m'dziko,

35. Kupambutsa ciweruzo ca munthu pamaso pa Wam'mwambamwamba,

Werengani mutu wathunthu Maliro 3