Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 3:17-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Watarikitsanso moyo wanga ndi mtendere; ndinaiwala zabwino.

18. Ndipo ndinati, Mphamvu yanga yatha, osayembekezanso kanthu kwa Yehova.

19. Kumbukirani msauko Wanga ndi kusocera kwanga, ndizo civumulo ndi ndulu.

20. Moyo wanga uzikumbukirabe nuwerama mwa ine,

21. Ndiri naco ciyembekezo popeza ndilingalira ici ndiyembekeza kanthu.

22. Cifukwa cakusathedwa ife ndico cifundo ca Yehova, pakuti cisoni cace sicileka;

23. Cioneka catsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.

24. Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova; cifukwa cace ndidzakhulupirira.

25. Yehova akhalira wabwino omlindirira, ndi moyo womfunafuna.

26. Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha cipulumutso ca Yehova.

27. Nkokoma kuti munthu asenze gori ali wamng'ono.

28. Akhale pa yekha, natonthole, pakuti Mulungu wamsenzetsa ilo.

29. Aike kamwa lace m'pfumbi; kapena ciripo ciyembekezo.

Werengani mutu wathunthu Maliro 3