Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 3:10-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Andikhalira cirombo colalira kapena mkango mobisalira.

11. Wapambutsa njira zanga, nanding'amba; nandipululutsa.

12. Wathifula uta wace, nandiyesa polozetsa mubvi.

13. Walowetsa m'imso mwanga mibvi ya m'phodo mwace.

14. Ndasanduka wondiseka mtundu wanga wonse, ndi nyimbo yao tsiku lonse.

15. Wandidzaza ndi zowawa, wandikhutitsa civumulo.

16. Watyolanso mano anga ndi tinsangalabwi, wandikuta ndi phulusa.

17. Watarikitsanso moyo wanga ndi mtendere; ndinaiwala zabwino.

18. Ndipo ndinati, Mphamvu yanga yatha, osayembekezanso kanthu kwa Yehova.

19. Kumbukirani msauko Wanga ndi kusocera kwanga, ndizo civumulo ndi ndulu.

20. Moyo wanga uzikumbukirabe nuwerama mwa ine,

21. Ndiri naco ciyembekezo popeza ndilingalira ici ndiyembekeza kanthu.

22. Cifukwa cakusathedwa ife ndico cifundo ca Yehova, pakuti cisoni cace sicileka;

23. Cioneka catsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.

24. Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova; cifukwa cace ndidzakhulupirira.

Werengani mutu wathunthu Maliro 3