Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 2:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Yehova wameza nyumba zonse za Yakobo osazicitira cisoni;Wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wace;Wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ace.

3. Pokwiya moopsya walikha nyanga zonse za Israyeli;Wabweza m'mbuyo dzanja lace lamanja pamaso pa adaniwo,Natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.

4. Wathifula uta wace ngati mdani, waima ndi dzanja lace lamanja ngati mmaliwongo;Wapha onse okondweretsa maso;Watsanulira ukali wace ngati moto pa hema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.

5. Yehova wasanduka mdani, wameza Israyeli;Wameza zinyumba zace zonse, wapasula malinga ace;Nacurukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi cibumo.

6. Wacotsa mwamphamvu dindiro lace ngati la m'munda;Waononga mosonkhanira mwace;Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi sabata m'Ziyoni;Wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.

7. Ambuye wataya guwa lace la nsembe, malo ace opatulika amnyansira;Wapereka m'manja a adani ace makoma a zinyumba zace;Iwo anaphokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.

8. Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni;Watambalika cingwe, osabweza dzanja lace kuti lisaonongepo;Waliritsa chemba ndi linga; zilefuka pamodzi.

Werengani mutu wathunthu Maliro 2