Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 8:2-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Tenga Aroni ndi ana ace pamodzi naye ndi zobvalazo, ndi mafuta odzozawo, ndi ng'ombe ya nsembe yaucimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi mtanga wa mkate wopanda cotupitsawo;

3. nusonkhanitse khamu lonse ku khomo la cihema cokomanako.

4. Ndipo Mose anacita monga Yehova anamuuza; ndi khamulo linasonkhana pa khomo la cihema cokomanako.

5. Ndipo Mose anati kwa msonkhanowo, Ici ndi cimene Yehova adauza kuti cicitike.

6. Ndipo Mose anabwera nao Aroni ndi ana ace, nawasambitsa ndi madzi,

7. Ndipo anambveka ndi maraya a m'kati, nammanga m'cuuno ndi mpango, nambveka ndi mwinjiro, nambveka ndi efodi, nammanga m'cuuno ndi mpango wa efodi nammanga nao pathupi pace.

8. Ndipo anamuika capacifuwa; naika m'capacifuwa Urimu ndi Tumimu.

9. Naika nduwirayo pamutu pace; ndi panduwira, pamphumi pace anaika golidi waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.

10. Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza kacisi, ndi ronse ziti m'mwemo, nazipatula.

11. Ndipo anawazako pa guwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zace zonse, ndi mkhate ndi tsinde lace, kuzipatula.

12. Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula,

13. Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawabveka maraya a m'kati, nawamanga m'cuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adauza Mose.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 8