Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 7:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. ndi imso ziwiri, ndi mafuta a pamenepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso;

5. ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe, nsembe yamoto ya kwa Yehova; ndiyo nsembe yoparamula.

6. Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulikitsa.

7. Monga nsembe yaucimo, momwemo nsembe yoparamula; pa zonse ziwirizi pali cilamulo cimodzi; ikhale yace ya wansembeyo, amene acita nayo cotetezera.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 7