Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 7:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo acotseko, nabwere nao mafuta ace onse; mcira wamafuta, ndi mafuta akukuta matumbo,

4. ndi imso ziwiri, ndi mafuta a pamenepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso;

5. ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe, nsembe yamoto ya kwa Yehova; ndiyo nsembe yoparamula.

6. Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulikitsa.

7. Monga nsembe yaucimo, momwemo nsembe yoparamula; pa zonse ziwirizi pali cilamulo cimodzi; ikhale yace ya wansembeyo, amene acita nayo cotetezera.

8. Ndipo cikopa ca nsembe yopsereza cikhale cace cace ca wansembe, amene anabwera nayo nsembe yopsereza ya munthu ali yense.

9. Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumcembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi paciwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo,

Werengani mutu wathunthu Levitiko 7