Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 7:26-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo musamadya mwazi uti wonse, kapena wa mbalame, kapena wa nyama, m'nyumba zanu zonse,

27. Ali yense akadya mwazi uti wonse, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.

28. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

29. Lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Wakubwera nayo nsembe yoyamika yace kwa Yehova, azidza naco copereka cace kwa Yehova cocokera ku nsembe yoyamika yace;

30. adze nazo m'manja mwace nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

31. Ndipo wansembeyo atenthe mafutawo pa guwa la nsembe; koma ngangayo ikhale ya Arent ndi ana ace.

32. Ndipo mwendo wathako wa ku dzanja lamanja muupereke kwa wansembe, ukhale nsembe yokweza yocokera ku nsembe zoyamika zanu.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 7