1. Ndipo cilamulo ca nsembe yoparamula ndi ici: ndiyo yopatulikitsa.
2. Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo aziphera nsembe yoparamula; nawaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.
3. Ndipo acotseko, nabwere nao mafuta ace onse; mcira wamafuta, ndi mafuta akukuta matumbo,
4. ndi imso ziwiri, ndi mafuta a pamenepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso;
5. ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe, nsembe yamoto ya kwa Yehova; ndiyo nsembe yoparamula.
6. Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulikitsa.