Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 5:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo akacimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osaulula, azisenza mphulupulu yace;

2. kapena munthu akakhudza ciri conse codetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa coweta codetsa, kapena mtembo wa cokwawa codetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi woparamula.

3. Kapena akakhudza codetsa ca munthu, ndico codetsa ciri conse akakhala codetsedwa naco, ndipo cidambisikira; koma pocizindikira akhala woparamula:

4. kapena munthu akalumbira ndi milomo yace osalingirira kucita coipa, kapena kucita cabwino, ciri conse munthu akalumbira osalingirira, ndipo cidambisikira; koma pocizindikira akhala woparamula cimodzi ca izi:

Werengani mutu wathunthu Levitiko 5