Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 3:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo abwere naco copereka cace cotengako, ndico nsembe yamoto ya kwa Yehova; acotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,

15. ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso.

16. Ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe; ndizo cakudya ca nsembe yamoto icite pfungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.

17. Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 3