Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 3:12-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo copereka cace cikakhala mbuzi, azibwera nayo pamaso pa Yehova;

13. naike dzanja lace pamutu pace, naiphe pa khomo la cihema cokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.

14. Ndipo abwere naco copereka cace cotengako, ndico nsembe yamoto ya kwa Yehova; acotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,

15. ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso.

16. Ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe; ndizo cakudya ca nsembe yamoto icite pfungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 3