Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 24:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2. Uza ana a Israyeli, kuti akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti aziwalitsa nyali nthawi zonse.

3. Aroni aikonze kunja kwa nsaru yocinga ya mboni, m'cihema cokomanako, kuyambira madzulo kufikira m'mawa, pamaso pa Yehova nthawi zonse; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu.

4. Akonze nyalizo pa coikapo nyali coona pamaso pa Yehova nthawi zonse.

5. Ndipo uzitenga ufa wosalala, ndi kuphika timitanda khumi ndi tiwiri; awiri a magawo khumi a efa afikane kamtanda kamodzi,

6. Ndipo utiike m'mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova.

7. Nuike libano loona ku mzere uli wonse, kuti likhale kumkate ngati cokumbutsa, nsembe yamoto ya Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 24