Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 23:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Nyengo zoikika za Yehova zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, ndizo nyengo zanga zoikika.

3. Masiku asanu ndi limodzi azigwira nchito; koma lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira nchito konse; ndilo sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.

4. Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, masonkhano opatulika, zimene muzilalikira pa nyengo zoikika zao.

5. Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mweziwo, madzulo, pali Paskha wa Yehova.

6. Ndipo tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi womwewo ndilo madyerero a mkate wopanda cotupitsa a Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda cotupitsa.

7. Tsiku lace loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira nchito ya masiku ena.

8. Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lacisanu ndi ciwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamacita nchito ya masiku ena.

9. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

10. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, ndi kuceka dzinthu zace, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe;

11. ndipo iye aweyule mtolowo pamaso pa Yehova, ulandirikire inu, tsiku lotsata sabata wansembe aweyule.

12. Ndipo tsiku loweyula mtolowo, ukonze mwana wa nkhosa wopanda cirema, wa caka cimodzi, akhale nsembe yopsereza ya Yehova.

13. Ndipo nsembe yaufa yace ikhale awiri a magawo khumi a ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ndiyo nsembe yamoto ya Yehova, icite pfungo lokoma; ndi nsembe yace yothira ikhale yavinyo, limodzi la magawo anai la hini.

14. Musamadya mkate, kapena tirigu wokazinga, kapena ngala zaziwisi, kufikira tsiku lomweli, kufikira mutadza naco copereka ca Mulungu wanu; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 23