Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 18:23-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo usamagonana ndi nyama iri yonse, kudetsedwa nayo; kapena mkazi asamaima panyama, kugonana nayo; cisokonezo coopsa ici.

24. Musamadzidetsa naco cimodzi ca izi; pakuti amitundu amene ndiwapitikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi;

25. dziko lomwe lidetsedwa; cifukwa cace ndililanga, ndi dzikoli lisanza okhala m'mwemo.

26. Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osacita cimodzi conse ca zonyansa izi; ngakhale wa m'dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu;

27. (pakuti eni dziko okhalako, musanafike inu, anazicita zonyansa izi zonse, ndi dziko linadetsedwa)

28. lingakusanzeni inunso dzikoli, polidetsa inu, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako musanafike inu.

29. Pakuti ali yense akacita ciri conse ca zonyansa Izi, inde amene azicita idzasadzidwa pakati pa anthu a mtundu wao.

30. Potero muzisunga cilangizo canga, ndi kusacita ziri zonse za miyambo yonyansayi anaicita musanafike inu, ndi kusadzidetsa nayo: Ine ndine Yehova Mulungu-wako.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 18