Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 18:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Ine ndine Yehova Molungu wanu.

3. Musamacita monga mwa macitidwe a dziko la Aigupto muja munakhalamo; musamacita monga mwa macitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao.

4. Muzicita maweruzo anga, ndi kusunga malemba anga, kumayenda m'mwemo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

5. Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawacita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.

6. Asasendere mmodzi wa inu kwa mbale wacekumbvula; Ine ndine Yehova.

7. Usamabvula atate wako, ndi mai wako; ndiye mai wako, usamambvula.

8. Usamabvula mkazi wa atate wako; ndiye thupi la atate wako.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 18