Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 15:30-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Ndipo wansembe apereke limodzi likhale nsembe yaucimo, ndi linalo likhale nsembe yopsereza; ndipo wansembe amcitire comtetezera pamaso pa Yehova cifukwa ca kukha kwace komdetsa.

31. Motero muzipatula ana a Israyeli kwa kudetsedwa kwao; angafe m'kudetsedwa kwao, pamene adetsa kacisi wanga ali pakati pao.

32. Ici ndi cilamulo ca wakukha, ndi ca iye wakugona uipa, kuti kumkhalitse wodetsedwa;

33. ndi ca mkazi alinkudwala ndi kudetsedwa kwace, ndi ca iye alikukha kapena mwamuna, kapena mkazi, ndi ca iye agona ndi mkazi wodetsedwa.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 15